Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 340

Paphata pa Chichewa Siigwira ayi: Sizitheka ayi. Chitsanzo: Nkhani mukunenayi siigwira ayi, ingoku- lowetsani m’mavuto. Sindimaimva: Sindimalola zachibwana. Chitsanzo: Wina akamafuna kundipusitsa sindimaimva, ndimamusonyeza kuti nanenso ndi duli. Sindimayenda: Ndimakonda kukhala pakhomo. Chitsanzo: Mukadzabwera tsiku lililonse mudzandipeza, sindimayenda ine. Sindinabwere kudzachititsa msonkhano: Sindinabwere kudzakhazikika, sindinabwere kudzachita zambiri. Chitsanzo: Sindinabwere kudzachititsa msonkhano, ndikungodutsa. Sindiona: Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene sa- matha kuwerenga m’malo mongonena kuti kusukulu sanapiteko. Chitsanzo: (1) Ngakhale muwapatse kalatayo palibe chimene angatolepo chifukwa samaona. (2) Mukawapatsa buku mungoononga, samaona. Sindyeka: Munthu wosatheka kumenyedwa. Chitsanzo: Amene ujatu ndi sindyeka, koma tsiku lina adzadyeka ndi mafupa omwe. Singano ndi ulusi: Kulikonse kumene winayo walowera mnzake amalowelanso komweko. Chitsanzo: Kuyambira lero tizikhala ngati singano ndi ulusi. Sisita: Gwira ntchito pang’onopang’ono. Chitsanzo: Anthu ena amadziwa ntchito ndithu, koma amangosisita. Sisitira bombono: Zengereza. Chitsanzo: Akafuna kuchita chinthu amakonda kusisitira bombono. 339