Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 34

Paphata pa Chichewa wamwini ndiye anthu apita kukakambirana za nkhaniyo kwa munthuyo. Anthuwo akafika, eni pakhomopo amanena kuti awalipire chikhalamumthunzi kuti amasuke kunena chomwe abwerera. Akapereka malipiro amenewa mpamene mlanduwo umayamba. Chitsanzo: Musananene zambiri, yambani kaye mwatipatsa chikhalamumthunzi. Chikhwaya: Munthu wolemera. Chitsanzo: Malo ano kumabwera zikhwaya zokhazokha. Chikondi cha bulangete: Chikondi chachikulu kwambiri. Chitsanzo: Chikondi cha amene aja ndi cha bulangete. Chikondi chobwerekana nsalu: Kugwirizana kwambiri. Chitsanzo: Chikondi chawo ndi chobwerekana nsalu. Chikulowa kudzino: Chikukopa moti uyamba kuchikonda kwambiri. Chitsanzo: Ukadzangodya bokho kamodzi, adzakulowa kudzino. Chikumbumtima: (a) Munthu wamkati amene amakuletsa ukamafuna kuchita zoipa komanso amakuimba mlandu ukalakwitsa. Chitsanzo: Atapha munthu, chikumbumtima chake chinayamba kumuvutitsa. (b) Kukumbukira zinthu. Chitsanzo: Mayi uja ali ndi chikumbumtima, ukamuuza zinthu saiwala. Chikwanekwane: Kusasowa kanthu. Chitsanzo: Ukamapita kutali umafunika kumayenda chikwanekwene. 33