Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 339

Paphata pa Chichewa (b) Kupha zonse kapena kuchotsa zonse. Chitsanzo: (a) Chitopa chasesa nkhuku zonse. (b) Matend- awa akhoza kusesa mudzi wonse. (c) Kuchotsa zinyalala ndi tsache. Chitsanzo: Sesani pabwalo padutse chintali. Sewera ndi pakamwa: Yankhula zinthu zoti ukhoza kupalamula nazo. Chitsanzo: Munthu ameneyutu akusewera ndi pakamwa, zoona kumanyoza mtsogoleri wadziko? Sewera paulimbo: Kuchitsa zinthu zomwe ukhoza kupalamula nazo, kuputa munthu. Chitsanzo: (1) Bambowa akusewera paulimbo, akachita masewera amangidwa. (2) Iwetu ukusewera paulimbo, akhoza kukuonetsa chinameta nkhanga mpala. Shasha (syasya): (a) Munthu wolemera. Chitsanzo: Usayese kupikisana mavalidwe ndi amene uja chifukwa ndi shasha. (b) Munthu wochangamuka kapena wochenjera. Chitsanzo: Awa ndi mashasha a m’tauni muno. Shomola nkhandwe: Palamula. Chitsanzo: Anyamata amene aja amupha, washomola nkhandwe. Shosholo: Kuyendera limodzi. Chitsanzo: Amayenda shosholo ndi akazi awo. Shupa: Kuvutitsa. Chitsanzo: Munthu ameneyu amandishupa kwabasi. Si masewera: Ndi patali, ali ndi luso kapena amachita bwino zinazake. Chitsanzo: Mwamuna wawo uja si masewera. Si zocheza: Ndi patali. Chitsanzo: Nsapatoyi si zocheza. 338