Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 338
Paphata pa Chichewa
Sauka:
(a) Kumwalira kwa wina wa m’banja.
Chitsanzo: Pakhomo pano tinasauka chipitireni
achimwene athu aja.
(b) Kutha kwa chuma, kukhala opanda ndalama.
Chitsanzo: Ambiri omwe anali olemera asauka.
(c) Kuvutika.
Chitsanzo: Akusaukabe ndi matenda aja.
Sawa:
(a) Kuwawa.
Chitsanzo: Simunabwere kudzationa moyo utasawa.
(b) Kufika povuta kwambiri.
Chitsanzo: Kuntchitoku kwasawa.
(c) Kukhala choti sichingapse, kukhala chamadzi ambiri.
Chitsanzo: Chinangwachi ndi chosawa.
Sekerera ku khudu: Sekerera utayang’ana kumbali.
Chitsanzo: Mukundinena eti? Nanga n’chifukwa chiyani
mukusekera ku khudu.
Sekereren’kudyeremwana: Munthu wachinyengo.
Chitsanzo: Amene uja ndi sekereren’kudyeremwana.
Seleula: Kunena munthu monyoza.
Chitsanzo: Ndinawapeza akuseleulana ndi alamu awo.
Senda: Menya kwambiri.
Chitsanzo: Akusendatu!
Sendera: Yandikira.
Chitsanzo: Sendera pafupi ndikunong’oneze.
Senza: Mwalira.
Chitsanzo: Amfumuwo azunzika kwa kanthawi, lero
asenza.
Sesa:
(a) Kufala, kukhudza ambiri.
Chitsanzo: Njala imene ija inasesa mudzi wonse.
337