Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 337
Paphata pa Chichewa
Sandiona bwino:
(a) Amaoneka kuti amadana nane.
Chitsanzo: Munthu ameneyu sandiona bwino.
(b) Amandikayikira.
Chitsanzo: Munthuyu sindimuona bwino.
Sanduka luzi: Kuonda kwambiri.
Chitsanzo: Msungwana ankapukusika uja
simungamudziwe lero, anasanduka luzi atatenga ka-
chilombo.
Sanduliza: Tembenuza, kusintha munthu.
Chitsanzo: Akufuna kukusandulizani.
Sangandithe: Sangandisinthe, sangalimbane ndi ine.
Chitsanzo: Ngakhale alimbane nane, sangandithe.
Saona ndi maso: Munthu wakuba.
Chitsanzo: Anthu ena saona chinthu ndi maso.
Saonandege: Nkhumba.
Chitsanzo: Akufuna ndikawakonzere saonandege.
Sapita m’thumba: Satulutsa ndalama.
Chitsanzo: Anthu ena akapita kumowa sapita m’thumba,
amangodikira kuti anzawo aziwagulira.
Sasatuka: Kuyerekedwa, kudzikweza, kudzimva.
Chitsanzo: Si kale pamene anayamba kusasatuka.
Sasira nkhani: Kunamizira munthu wina wosalakwa.
Chitsanzo: Munthuyu ndi wosalakwa, nkhaniyi angomu-
sasira.
Sasunga pakamwa: Munthu wosabisa kanthu kapena
wosasunga chinsinsi.
Chitsanzo: Amene ajatu satha kusunga pakamwa.
Satha phazi: Amabwera kawirikawiri.
Chitsanzo: (1) Waona chiyani kuti asamathe phazi
pakhomo pano. (2) Achimwene anu satha phazi pakhomo
pano.
336