Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 334

Paphata pa Chichewa Pwepwete: (a) Munthu wolemera. Chitsanzo: (1) Dera lino kumakhala mapwepwete. (2) Anzanu anakwatiwa ndi pwepwete. (b) Kuseka. Chitsanzo: Ndinawapeza ali pwepwete! Pwetedza (pwepweta): Kudya, kutswa fupa. Chitsanzo: Akupwetedza (pwepweta) mafupa. Pya: Kungoyepula, kungodutsa pamwambamwamba. Chitsanzo: (1) Sanafotokoze zambiri, anangoti pya! (2) Anatigawira chochepa, moti pamene amapakula anangoti pya! 333