Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 332

Paphata pa Chichewa Psinja (psinjana): Panikiza, panikizana. Chitsanzo: (1) Mavuto amupsinja. (2) Anthu amenewa amapsinjana. Psipitsa mpani: Bera munthu, kutengera munthu wina chinthu. Chitsanzo: Mnzake uja ndi amene wamupsipitsa mpani. Psitiriza: Pondereza. Chitsanzo: Akuluakulu aboma akumangopsitiriza am- phawi. Psota: Kumenyedwa kwambiri. Chitsanzo: Anzake amupsota kwambiri. Psuta: Munthu wakuba. Chitsanzo: Tam’pusitsa psuta uja. Pukusa mutu: Kukana. Chitsanzo: Atamufunsa anangopukusa mutu. Pukusika: Kuyenda monyada. Chitsanzo: Kodi mukudzizunziranji pomayenda mopukusika apa? Palibetu angakufunsireni pano! Pulula: (a) Kulephera. Chitsanzo: Wapulula, amaganiza kuti agwira! (b) Kumaliza zonse ngakhale zosakhwima, kupha onse. Chitsanzo: Matenda a edzi akupulula miyoyo ya anthu. Pululu: Posatseka. Chitsanzo: Anangosiya kukhomo kuli pululu. Puma fwekufweku: Matenda oti mwina sachira, kuvutika kupuma. Chitsanzo: Sali bwino mpangono pomwe, akungopuma fwekufweku. Puma kupha nyerere: Kusiya kuyenda wapansi, kuyenda pagalimoto kapena njinga. Chitsanzo: Lero ndipumeko kupha nyerere. 331