Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 331

Paphata pa Chichewa Ponya nkhwanga n’chambuyo: Ndi osabereka kapena kuti chumba. Chitsanzo: Amene aja anaponya nkhwangwa n’chambuyo, n’chifukwa chake m’nyumba mwawo mulibe wailesi. Ponya patsogolo: Thandiza. Chitsanzo: Ndimasowa mtengo wogwira moti mwandiponyera patsogolo. Ponya sitepe: Vina. Chitsanzo: Ndinadabwa nditamuona akuponya sitepe pa ukwati. Potola: Kupha. Chitsanzo: Amene wandibera miyono yanga wandipotola. Potoza: Kusemphanitsa zinthu, kuvala nsapato mwendo womwe si wake, kuchita zinthu mosayenera. Chitsanzo: (1) Mwanayu wapotoza nsapato. (2) Anthuwa amapotoza mawu a Mulungu kuti zigwirizane ndi mfundo zawo. Psanga: Kuba, kutenga zambiri kuposa ena. Chitsanzo: (1) Zonse zomwe ali nazozi n’zopsanga. (2) M’malo moti tigawane mwachilungamo akumangopsanga. Psereza nalo bodza: Namiza kwambiri. Chitsanzo: Iye amangomvetserabe, samadziwa kuti akumupsereza nalo bodza. Psete: (a) Kuyankhula mosaopa, mosabisa mawu. Chitsanzo: (1) Amayankhula mopanda psete. (2) Bamboyu alibe psete. Ponda pamutu: (a) Kubadwa pambuyo pa woyamba. Chitsanzo: Mwana uyu anaponda pamutu pa uyu. (b) Nyoza. Chitsanzo: Ife ndiye amangotiponda pamutu. 330