Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 327

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Ntchito yosoka nsapato ndi chisongole si- funa munthu waphuma. (2) Mnyamatayu ndi waphuma. Phunzi: Phewa. Chitsanzo: Bwera ndikunyamule paphunzi. Phuvumula: Menya koopsa. Chitsanzo: Chimunthu chimenechi n’chofunika kuchiphuvumula. Phwamwamwa: Zochuluka zedi, zambirimbiri. Chitsanzo: Pakhomo pawo zakudya zili phwamwamwa. Phwando ladzaoneni: Phwando lalikulu. Chitsanzo: Anachita phwando ladzaoneni. Phwanya: (a) Chakudya. Chitsanzo: Lowanitu, muli phwanya m’nyumbamu. (b) Menya modyetsa nkhawa, menya koospa. Chitsanzo: Ukuchita makani, ndikuphwanyatu! Phwasula: Menya koopsa, panda. Chitsanzo: Akachita masewera ndimuphwasula. Phwete: Kuseka kwambiri. Chitsanzo: (1) Musandipangitse phwete. (2) Mwanayu ndi waphwete. Phwetsa m’khuto: Kupuma utamaliza kudya. Chitsanzo: Ndikakhala pampando wa ndakhuta ndalema kuti ndikaphwetse nkhuto. Phwintha: Kuunjiza kapena kuika zambirimbiri. Chitsanzo: (1) Ndiwozi aziphwintha mchere. (2) Nsimayi mwaiphwintha ufa. Pikitipikiti (pichikapichika): Kuyendayenda kwa anthu. Chitsanzo: Anthuwo amangoti pikitipikiti. Pinda mchira: Kuchita mantha. Chitsanzo: Zinthu zikavuta chonchi ambiri amangopinda mchira n’kuthawa. 326