Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 326

Paphata pa Chichewa (b) Kulimbana, kusamvana. Chitsanzo: Pakati pawo pali phote. Phovomora: Kumenya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Mkazi wa m’kamwa uja anamuphovomora dzu- lo. Phukusi: Chinthu chokulungidwa munsalu kapena chinachake. Chitsanzo: Nyamulani kaphukusi kanuka. Phula ngozi: Menya munthu, vulaza munthu, chita ngozi. Chitsanzo: Mutengeni mwana wanuyu akhoza kundiphu- litsa ngozi. Phula utsi: Kunena zinthu zimene sukuzimvetsa. Chitsanzo: Mayi aja amaphula utsi. Phula: (a) Munthu wopusa. Chitsanzo: Sukulu imafuna mwana wochangamuka osati phula. (b) Kupeza chuma. Chitsanzo: Anzanu aja anaphula. (c) Kuchotsa chinthu pamoto. Chitsanzo: Aphula nyemba zosapsa. Phuliphuli: Kukongola, kuoneka bwino. Chitsanzo: (1) Phuliphuli si njinga koma tcheni. (2) Phu- liphuli ameneyu mukulowera kuti? Phulitsa: Menya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Wayambanso kugeya mwano, ndikhoza ku- kuphulitsatu! Phulusika: Kukalipa. Chitsanzo: Ndinawapeza akuphulusika, maso ali piriwiri ndi ukali. Phuma: Kuchita zinthu mosaganiza bwino, wopupuluma pochita zinthu, wolongolola. 325