Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 325
Paphata pa Chichewa
Phimba m’maso: Namiza.
Chitsanzo: Musadzalole kuti akuphimbeni m’maso.
Phinya: Panikiza kwambiri.
Chitsanzo: Kuti aulure mpofunika kumuphinya.
Phoda: Dzola zokongoletsa.
Chitsanzo: Akaphoda amangooneka ngati chilombo.
Phokonyole: Chinthu chakutha, chakale.
Chitsanzo: Agula phokonyole wawo kuti apume kuyenda
wapansi.
Phokonyole: Galimoto, njinga kapena chinthu china
chakutha.
Chitsanzo: Kodi kaphokonyole kanu kaja kali kuti?
Phokoso:
(a) Kulongolola, kusokosa.
Chitsanzo: (1) Pasapezeke munthu wopanga phokoso
m’kalasi muno! (2) Ana amene amapanga phokoso
anawagwiritsa chibalo.
(b) Fungo loipa, kununkha.
Chitsanzo: (1) Ndi sokosi za ndani zikupanga phokosozo?
(2) Sokosi zake zimapanga phokoso.
Phoma bodza: Kunamiza munthu.
Chitsanzo: Nanunso anakuphoma naloni bodza.
Phonya: Lephera, lakwitsa.
Chitsanzo: Pepani ndinaphonya m’kalankhulidwe.
Phoso:
(a) Chakudya.
Chitsanzo: Ndatenga kaphoso.
(b) Katundu.
Chitsanzo: Anabwera ndi kaphoso ka chimanga.
Phote:
(a) Mavuto.
Chitsanzo: Pamudzipa pali phote.
324