Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 324
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Anangodziponya m’madzi kuti phava!
Phava: Zinthu zambiri, la nthochi.
Chitsanzo: (1) Amumenya kaphava ka makofi. (2) Eko
phava la nthochi.
Phazi limodzi: Mwamantha.
Chitsanzo: Pakhomo paja ndimapita ndi phazi limodzi.
Phazi ndiombole: Kuthawa.
Chitsanzo: Ukaona kuti zavuta umafunika kungopempha
kuti phazi likuombole.
Phazi thandize: Kuthawa zitavuta.
Chitsanzo: Zitavuta ndinangoti phazi thandize.
Phazi: Kuyenda kapena kupita kwinakwake.
Chitsanzo: Phazi lako lisamapitepite kwa mnzako chifu-
kwa akhoza kutopa nawe n’kuyamba kunyansidwa nawe.
Pheka: Kutheka, kugwidwa.
Chitsanzo: Wakuba amavuta uja lero wapheka.
Pheramphongo: Kutsirira ndemanga pankhani, kugwiri-
zana ndi zimene wina wanena.
Chitsanzo: Ndikufuna kupheramphongo zimene
achikulirewo anena.
Pherera: Kudziteteza, kudzitchinjiriza.
Chitsanzo: Amawayankha mowapherera.
Phesi. Munthu wopanda mphamvu.
Chitsanzo: Ukakhala phesi ndi bwino kungokhala chete
poopa kudziputira mavuto.
Phethira: Kungopusa pang’ono.
Chitsanzo: Mukaphethira akuyeretsani m’maso.
Phika maso: Kunyada kwambiri.
Chitsanzo: Atsikana a masiku ano ukawauza nkhawa za-
ko, akumangophika maso kenako n’kukutsonya.
323