Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 323

Paphata pa Chichewa Pepetula: Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito ponena za zikhulupiriro zomwe anthu a ku Africa kuno amakhala nazo zoti anthu amatha kulodzana kapena kuchitisa kuti wina akumane ndi tsoka. Chitsanzo: Sakumva masiku ano, akungokhala ngati amupepetula. Perekeza ndi maso: Kuyang’ana munthu moloza kumene akulowera. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani amandiperekeza ndi maso? Perekeza: Kutuma munthu komwe amakonda kupitako. Chitsanzo: Iyeyu anaonako kadona kumeneko, ndiye ku- mutumanso komweko n’kumuperekeza. Peremende: Mwamuna wadazi lalikulu. Chitsanzo: Mnyamata uyu ali ndi masweswe aakulu. Akadzakula adzakhala peremende. Petapeta: Kuweramawerama. Chitsanzo: (1) Udzu unkangoti petapeta. (b) Akamayenda amangoti petapeta. Phala: (a) Kuyankhula zopanda nzeru. Chitsanzo: Mwayakhulazitu ndi phala lenileni. (b) Chakudya choundana chamadzimadzi. Chitsanzo: Andiphikira phala lampunga. Phamula: Pakula zonse, tenga zonse. Chitsanzo: Ndani waphamulamo ndiwo zija? Phamuphamu: Zambirimbiri. Chitsanzo: Akati akugawire amangokupatsa phamuphamu. Phava: (a) Ndi dzina lotchulira zinthu zambiri monga nthochi. Chitsanzo: Andipatsa phava limodzi la nthochi. (b) Mvekero wa chinthu chomwe chagwera m’madzi. 322