Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 321
Paphata pa Chichewa
Pansi pamtedza: Chenjerani, kapena thawani.
Chitsanzo: Zinthu zavuta, pansi pamtedza!
Pansi pamtima:
(a) Chenicheni chimene munthu akufuna koma sa-
kuyankhula.
Chitsanzo: Ndinamuuza kuti sindikufuna ngakhale kuti
pansi pamtima ndimafuna.
(b) Mmene ukumvera mumtima mwako.
Chitsanzo: Amayankhula kuchokera pansi pamtima.
Pantondo: Pagulu.
Chitsanzo: Nkhani za m’banja mwana zimathera pan-
tondo.
Panyansa: Paipa.
Chitsanzo: Nditaona kuti panyansa, ndinangochokapo.
Panyekanyeka: Pamatilesi, pofewa.
Chitsanzo: Ana a mabwana amagona panyekanyeka.
Paphata: Pachimake pa zinthu.
Chitsanzo: Apa ndiye paphata pa makhalidwe oipa. (2)
Zulani phata la chinagwali.
Papira mowa: Kuledzera, kumwa mowa wambiri, ku-
gugudiza mowa.
Chitsanzo: Anangogwira botolo la mame n’kupapira mowa
wonse.
Pasambira mfulu: Kupeza zabwino chifukwa choti ena
ochita bwino apeza zinthuzo, kudya nawo.
Chitsanzo: Lero ndinayenda ndi bwana uja ndipo ena
anatiitanira mpunga. Inenso ndinangoti pasambira mfulu!
Patali: Si masewera, ndi mwamuna.
Chitsanzo: Achimwene anu aja ndi patali.
Patelera: Pavuta.
Chitsanzo: (1) Ndinangothawapo nditaona kuti patelela.
(2) Atabwera bambo, pakhomo panatelera.
320