Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 320
Paphata pa Chichewa
Pamoto: Pamavuto.
Chitsanzo: Amene wabetsa njinga ya agogo ali pamoto.
Pamphambano: Pokumana njira.
Chitsanzo: Agwirizana kuti akakumana pamphambano.
Pampondachimera: Pachimake, posangalatsa.
Chitsanzo: Mpikisano wafika pampondachimera.
Pamwera galu: Kulibe kapena kuti zatha.
Chitsanzo: “Kodi ntchito ija mwaipeza?” “Ayi kwamwera
galu.”
Panaterera: Panavuta.
Chitsanzo: Atangobwera achikulirewo panatelelera.
Pandime: Mawu otanthauza kukupeza ukugwira ntchito.
Chitsanzo: Anadipeza ndili pandime.
Panga munthu zoopsa: Khaulitsa.
Chitsanzo: Akakupezani akupangani zoopsa.
Panga phada: Kuchita masewera.
Chitsanzo: (1) Munthu wamkulu ngati ine sindingakhale
pano n’kumapanga phada. (2) Mukayamba kupanga pha-
da akuchotsani ntchito.
Panga zisanu: Kusintha zimene unanena.
Chitsanzo: Dzulo unalonjeza kuti ubwera, koma lero
wayamba kupanga zisanu.
Pangitsa chizungulire: Kuona zinthu ngati zikuzunguli-
ra, kusokoneza munthu.
Chitsanzo: Tangonenani, mpaka muchite kutipangitsa chi-
gungulire.
Panikiza ndi mafunso: Kufunsa mafunso mosalekeza.
Chitsanzo: Osandipandikiza ndi mafunso! Ngati mukufuna
kudziwa zonse pitani komweko!
Pansengwa panu: Anzanu.
Chitsanzo: Zimenezi ndi zimene amakonda kuchita
pansengwa pawo.
319