Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 32

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Achidyamakanda samalakwa, amalakwa ndi anawa. Kususukira tchipisi. Chidzadziwe n’chipande powomola: Aliyense adzalandira mphoto yomuyenera. Chitsanzo: Amene akuchita ulesi adzadya ulesi wawo womwewo. Chidzadziwe n’chipande powomola. Chidzam’mphepo: Munthu wofika mosayembekezereka kapena wobwera asanaitanidwe. Chitsanzo: Chitani changu, angatipeze chidzam’mphepo. Chidzete: Munthu wopusa, chitsiru. Chitsanzo: (1) Panopa mpamene ndazindikira kuti munthu uja ndi chidzete. (2) Chimenechi ndi chidzete. Chidzika: Kumangokhala osachitapo kanthu, kudikiriritsa munthu wina. Chitsanzo: Si bwino kumangochidzika mtsikana, osamufunsira. Chifunga: (a) Nkhungu ya mitambo. Chitsanzo: Kunjaku kwachita chifunga. (b) Tiyi wosakwanira mkaka. Chitsanzo: Anatipatsa tiyi wachifunga. Chifwamba: Kubisalira ena kuti uwabere, umbanda. Chitsanzo: Muthengo limeneli mukumabisala achifwamba. Chifwirimbiti: (a) Kudutsa kwa nthawi. Chitsanzo: Chifwirimbiti cha nthawi chikadutsa, nkhaniyi iyiwalika. 31