Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 318

Paphata pa Chichewa Pakamwa padzaulukira mbereswa: Udzapalamula. Chitsanzo: Osamangoyankhulayankhula pakamwa pangaulukire mbereswa. Pakamwa papite mphepo: Kukhalako osadya. Chitsanzo: Mwana ameneyu safuna kuti pakamwa pake papite mphepo. Pakamwa podya therere: Wonama. Chitsanzo: Osamakhulupirira zimene amakuuzani, pakamwa pake m’podya therere. Pakamwa podya zamchere: Munthu ukhoza kulakwitsa m’kayankhulidwe kapena kunena bodza. Chitsanzo: Muzingotikhululukira, apa ndi pakamwa podya zamchere. Pakamwa: (a) Munthu wodziwa kuyankhula Chitsanzo: Amene uja ndi wochenjera pakamwa. (b) Wolongolola. Chitsanzo: Mwana uyu ndi wapakamwa. Pakati: Kuyembekezera mwana. Chitsanzo: Azimayi apakati amafunika kumapita ku- chipatala nthawi zonse. Pakhonde: Nthawi yolira maliro, achibale ndi ena apafupi amapatsidwa malo oti agone ndipo nthawi zambiri pamakhala pakhonde. Chifukwa cha zimenezi, pakhomo anthu akapita kukagona kumaliro kaya agona m’nyumba, amangoti adagona pakhonde. Chitsanzo: Mfumu itamwalira, anthu adagona pakhonde masiku awiri. Pakhota mchira wanyani: Pamene pali vuto. Chitsanzo: M’malo momangokangana, tiyeni tiyambe taona kaye pakhota mchira wanyani. 317