Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 314

Paphata pa Chichewa Onekera chimphonongolo: Pusa. Chitsanzo: Amafuna azioneka ochenjera kwinaku akuon- ekera chimphonongolo. Onekera matumbo: Wonyozeka ndi wopanda mphamvu. Chitsanzo: Kodi munthu woonekera matumbo uja angamenye munthu? Onekera uchitsiru: Kupusa. Chitsanzo: Apa ndiye mwaonekera uchitsirutu. Onera pakhosi: Matenda oti mwina sachira. Chitsanzo: Tinapita kukawaona, komatu timangoonera pakhosi kuti ali moyo. Onerana m’madzi (kuyang’anirana m’madzi): Kudana, kusalemekezana. Chitsanzo: Mbewa ndi zimene zinachititsa kuti ayambe kuonerana m’madzi. Onetsa chinameta nkhanga mpala: Menya kwambiri, onetsa zakuda. Chitsanzo: Ukadzabanso mango mumtengo wangawu, ndi- dzakuonetsa chinameta nkhanga mpala. Onetsa dzino (mano): Sekerera. Chitsanzo: Sindinamuonepo akuonetsa dzino. Onetsa miyendo: Ulula zinazake, kuchititsa kuti nkhani kapena chinachake chionekere poyera. Chitsanzo: Muzichita zinthu mosamala, tisachite kuonetsa miyendo. Onetsa nkolokolo: Kupusa. Chitsanzo: Bambowa amayankhula ngati anzeru kwinaku akuonetsa nkolokolo. Onetsa polekera: Mavuto osaneneka, khaulitsa. Chitsanzo: Akabweranso mowa uli m’mutu ndimuonetsa polekera. 313