Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 313
Paphata pa Chichewa
Omba ng’oma yowambawamba: Chitira wina chinthu
chimene amafuna kale kuti wina amuchitire.
Chitsanzo: Atandifunsa ngati ndikufuna kuvina,
ndinawauza kuti aomba ng’oma yowambawamba.
Ombera kuphazi: Kuthokoza kwambiri.
Chitsanzo: Tinaombera kuphazi apongozi atatitumizira
thumba la chimanga.
Ombera mapira pamutu: Chenjerera, chenjeretsa,
pusitsa.
Chitsanzo: Talima ndife, koma akungotiombera mapira
pamutu.
Ona bwino: Tisamaiwale kuthokoza amene atithandiza
mosayembekezereka.
Chitsanzo: Munthu wina akakugwiritsa kenakake, umafu-
nika kuyamba kuona bwino.
Ona mbwadza: Kukhaulitsidwa.
Chitsanzo: Mnyamata wakuba uja waona mbwadza ata-
mubudula zala.
Ona ndi maso: Kuona wekha.
Chitsanzo: (1) Ndinawaona ndi maso angawa. (2) Ndipita
kuti ndikaone ndi maso.
Ona nsana wanjira: Bwerera kwanu, kunyamuka n’ku-
mapita kumene wachokera.
Chitsanzo: Kunjaku kwada, tsopano ndione nsana wan-
jira.
Ona nyatwa: Kukhala m’mavuto.
Chitsanzo: Achimwene anu aja aona nyatwa akapanda
kubweza ngongole.
Ona zakuda: Kukumana ndi mavuto osaneneka, kukhau-
la.
Chitsanzo: Akadzabweranso adzaona zakuda.
312