Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 312

Paphata pa Chichewa Odalirika: Munthu amene sangakugwiritse mwala. Chitsanzo: Uyu ndi munthu wodalilika. Okanika: Osamva, osathandizika. Chitsanzo: Anthu ake ndi okanika, kuwalangiza samva. Okhupuka: Olemera. Chitsanzo: Banja lawo lonse ndi lokhupuka. Okungana: Ovuta. Chitsanzo: Ndikukumana ndi mavuto okungana. Olimba: Opirira, amphamvu. Chitsanzo: (1) Mwana uyu ndi wolimba. (2) Anthu a m’dera limeneli ndi olimba. Oloka: Kumaliza kusamba komwe ndi matenda amene akazi amadwala mwezi ndi mwezi. Chitsanzo: Ndinaoloka masiku awiri apitawo. Olokera pa kangaude: Kuchita mwayi utakumana ndi mavuto oti sukanapulumuka. Chitsanzo: Anangotsala pang’ono kundigwira moti ndangoolokera pakangaude. Olotsa azungu: Kazinga chimanga. Chitsanzo: Uzani alendowa azipita kuti ife tiolotse azungu. Olowa: Kufewa. Chitsanzo: Mpunga unaviika uja wawolowa. Omba bumi: Peza palibe. Chitsanzo: Anandiuza kuti chimanga chilipo, koma nditafika ndinaomba bumi chifukwa ndinachipeza chitatha. Omba khoma: Kupita kwina n’kusapeza zimene ukufuna. Chitsanzo: Ndimaganiza kuti ndikawapeza ali pakhomo, koma ndaomba khoma. Omba mfuti: Kuchita choipa. Chitsanzo: Mwana wa a Nasiyani waomba mfuti. 311