Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 310
Paphata pa Chichewa
Nyota:
(a) Mawu achipongwe kwambiri onena za munthu amene
akulira.
Chitsanzo: Ndani akunyota kuseriyo?
(b) Kabatani kaulemu komwe asilikali amalandira.
Angatanthauzenso kupatsidwa ulemu.
Chitsanzo: Mkulu uja walandiranso nyota ina.
Nyowa: Kuchita manyazi aakulu.
Chitsanzo: Mnyamata wochenjeretsa uja ananyoweratu
atamugwira ataba 50 kwacha.
Nyumba yaikulu: Kuchimbudzi.
Chitsanzo: Akatuluka kunyumba yaikulu, mukawatsirire
madzi osamba m’manja.
Nyumba yodontha: Wolongolola kwambiri.
Chitsanzo: Akazi awo aja ndi nyumba yodontha.
Nyumwa: Kuioperera, kukaikira, kukana.
Chitsanzo: Ndinainyumwa atandiuza akalandira ndalama
sabweza.
Nyung’unya:
(a) Kuwawasa.
Chitsanzo: Mandimuwa akunyung’unya.
(b) Kukuvutitsa maganizo, kungofuna kukupweteketsa
mtima.
Chitsanzo: (1) Akumadutsa ndi kanjinga kawo kaja kuti
atinyung’unyemo. (2) Sindingamufunsire, ndimangofuna
kumunyung’unya.
Nyungu kubalira kumphuno: Kuchitika potsiriza.
Chitsanzo: Zaka zonsezi ndakhala ndikusowa zinthu
zimenezi, ndiye n’kuzipeza pano ndithu! Nyungu yabalira
kumphuno.
Nzama m’kamwa nde: Kusowa mawu onena.
Chitsanzo: Atamufunsa kuti anenepo maganizo ake,
anangoti nzama m’kamwa nde!
309