Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 309

Paphata pa Chichewa Nyenyeswa: Tiziduswa ta chakudya kapena zinthu zina. Chitsanzo: Angondisiyira nyenyeswa za buledi. Nyenyezi: Atsikana okongola. Chitsanzo: Mnyamata wamfupi uja wagwira kanyenyezi kapamtundapo. Nyika: (a) Kunama Chitsanzo: Koma zimenezi n’zoona, sakutinyika ameneyu? (b) Kuchita zosalongosoka, kuwononga zinthu. Chitsanzo: (1) Ntchito ija angonyika. (2) Ndimaopa kuyankhula kuopa kuti ndinganyike. Nyimbo yafika patisowe: Yafika pakolasi. Chitsanzo: Nyimboyo itafika patisowe, anthu anachita kuwelama nayo dansi. Nyinyirika: Kuchita zinthu mokakamizika, kusafuna kuchita chinthu. Chitsanzo: Mwanayu akumanyinyirika ndikamutuma. Nyivula: Chita mwano, kupinda milomo moonetsa mwano. Chitsanzo: Anthu onse omwe anali pamwambowo anayamba kunyivula, ataona kuti mfumuyo ikuyankhula zopanda nzeru. Nyodola: Nyoza. Chitsanzo: Utangochoka muja anayamba kukunyodola. Nyominyomi: Kuyenda mowerama, mwamantha kapena mwaulemu. Angatanthauzenso kuyenda modzichepetsa. Chitsanzo: Anyamata ena akaona mtsikana amangoti nyominyomi pambuyo pake. Nyontcholi (nyontchololo): Kunyowa. Chitsanzo: Ndinawapeza ali nyontcholi. Nyota yong’alula kukhosi: Ludzu. Chitsanzo: Tigaireni madzi, nyota yang’alula kukhosi. 308