Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 308

Paphata pa Chichewa Nyanyala: Kukana kuchita zinthu, kukwiya. Chitsanzo: Anamunena ndiye wanyanyala. Nyatwa: Mawuwa amanenedwa potamanda chinthu kuti chili bwino kwambiri. Chitsanzo: Njinga imeneyi ndi nyatwa. Nyau: (a) Munthu wosaoneka bwino. Chitsanzo: Tachionani chinyau chikubwera apocho. (b) Gule. Chitsanzo: Chinyau chikuvina kunsewuko. Nyazitsa: Kunena zoipa zokhudza munthu kapena chin- thu. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani mukunyazitsa dzina langa. Nyengana: (a) Kunamizana. Chitsanzo: Ananyengana kudya galu. (b) Kuchita chiwerewere. Chitsanzo: Abusa akulalikira kutsogolowo anawagwira akunyengana ndi nkhosa yawo. Nyengerera: Kopa munthu, kambirana naye kuti achite zimene ukufuna. Chitsanzo: Gomonda amandinyengerera kuti ndimugulitse njinga. Nyengo ya masika: Nyengo yomwe anthu amagawana zinthu, nyengo yomwe anthu amakolola mbewu za- kumunda. Chitsanzo: Nyengo ya masika yafika tinenepe. Nyengo yachisanu: Nyengo yozizira yomwe kumagwa timawawa. Chitsanzo: Nyengo yachisanu imandisangalatsa. Nyenwa: Ali ndi nsanje. Chitsanzo: Mayiwa ali ndi nyenwa. 307