Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 307
Paphata pa Chichewa
Nyambo: Kachakudya komwe anthu amaika pamsampha
kapena pambedza kuti nyama kapena munthu akopeke.
Mawuwa amakhala chining’a tikawagwiritsa ntchito
potanthauza chinthu chimene chimaikidwa penapake
kapena kuchitidwa kuti chikope wina.
Chitsanzo: (1) Mayesero alionse amakhala ndi nyambo. (2)
Sungaphe nsomba popanda nyambo.
Nyamu:
(a) Ngumbi.
Chitsanzo: Lero tidyera nyamu.
(b) Mvekero wosonyeza kunyamuka.
Chitsanzo: Ataona kuti nyerere zawakwera anangoti nya-
mu!
Nyanga:
(a) Zinthu zomwe zimakhala pamutu pa nyama.
Chitsanzo: Mbuzi ili ndi nyanga ija yathyoka mwendo.
(b) Zithumwa, nsupa.
Chitsanzo: Munthu ameneyu amadalira nyanga.
(c) Munthu wokhwima, mfiti.
Chitsanzo: Munthu ameneyu ndi wanyanga.
Nyangu: Manthongo oyera a m’maso.
Chitsanzo: Sindifuna mwamuna wa nyangu.
Nyani: Mawuwa amanenedwa akamanyoza munthu
yemwe si wooneka bwino.
Chitsanzo: Munyimbo ina mtsikana ankanyoza mnyamata
pomuuza kuti, ‘Unali ndani iwe! Tinkadabwatu kuti kodi
nyani ameneyu ndi wa ndani?’
Nyansi: Matudzi, bibi, manyi, matope, zinthu zoipa.
Chitsanzo: Ndaponda nyansi.
Nyansi:
(a) Manyi, bibi.
Chitsanzo: Nyansi zili kuserizo ndi za ndani?
(b) Uve, zopanda ukhondo, zalitsiro.
Chitsanzo: Kapuyitu ili ndi nyansi.
306