Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 305

Paphata pa Chichewa Nthongo: (a) Mbamu. Chitsanzo: Uzitemba nthongo zogwirizana ndi msinkhu wako! (b) Zinthu zomwe zimatuluka m’mbali mwa maso. Chitsanzo: Tamuchotsani manthongo mwanayo. Nthongo: Mbamu. Chitsanzo: Ndani wanditengera nthongo yanga? Nthuku: Mtima wokwiya. Chitsanzo: Atayamba kubweza moto, mtima wangawu unachita nthuku ndipo ndinkafuna kumupanda. Nthuli: Nyama yophikidwa yomwe ndi yoduladula. Chitsanzo: Aliyense atenge nthuli imodzi. Nthumanzi: Mantha. Chitsanzo: Zimene achitazi zandichititsa nthumanzi. Nthumbi: Kumwalira kwa mkazi pa nthawi yobereka, maliro a mkazi wapakati. Chitsanzo: (1) Mkazi wake anamwalira nthumbi. (2) Maliro achitika pamtundapo ndi a nthumbi. Nthumbidwa: Mwana wamng’ono amene pamutu pake padaponda winanso wakhanda, kapena mwana wakhanda pamene mayi wake ali ndi pakati. Chitsanzo: Sabata yatha tinakazonda matenda. Imadwala ndi nthumbidwa yawo ija. Nthumwi: Munthu wotumidwa kukachita zinazake kapena kukaimira munthu wina. Chitsanzo: Atumiza nthumwi yawo. Nthutumba: Chiwalo cham’mimba chomwe chimakhala ndi nchenga mkati. Chitsanzo: Ine ndidyera nthutumba. Nthyamba: Munthu waulesi. Chitsanzo: Ndani angasunge nthyamba pakhomo pake? 304