Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 304

Paphata pa Chichewa Nthawi yachikuda: Nthawi yochedwa, kuchita zinthu mochedwa, mosagwira nthawi. Chitsanzo: Ife timayendera nthawi yachikuda. Nthawi yochira: Nthawi yobereka mwana. Chitsanzo: Ikakwana nthawi yochira pamafunika kuchita zinthu mosamala. Nthawi yoipa: Nthawi yosayenera kuchita zinthu, nthawi ya mavuto. Chitsanzo: Zinthu zimenezi zabwera pa nthawi yoipa. Nthawi yotaika: Mochedwa, kuchedwa. Chitsanzo: Anabwera nthawi yotaika. Nthawi yowawitsa: Nthawi yovuta. Chitsanzo: Tikukhala munthawi yowawitsa. Nthawi yoyamba: Koyamba, ulendo woyamba. Chitsanzo: Ino ndi nthawi yoyamba kukumana nawo. Nthenda ya kumwezi: Khunyu. Chitsanzo: Akazi awo aja amadwala nthenda ya kumwezi. Ntheng’eneng’e: Kuchititsa mantha. Chitsanzo: Munthu emeneyu amandipatsa ntheng’eneng’e. Ntheradi: Ndithudi. Mawuwa amanenewa potsindika kuti zimene ukunena ndi zoona. Chitsanzo: Ntheradi, anandiuza kuti akubwera! Nthetemya: Mawu osalala, mawu abwino. Chitsanzo: Akazi amakhala ndi mawu a mthetemya. Nthiti: (a) Mkazi. Chitsanzi: Ndipite kumudzi ndikatenge nthiti yanga. (b) Mafupa a pachifuwa. Chitsanzo: Anachita ngozi moti wathyoka nthiti zitatu. 303