Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 302

Paphata pa Chichewa mphamvu pamudzi wachikamwini. Ntchenzi m’mbuyo: Kusintha zomwe unayankhula. Chitsanzo: Osamachita ntchenzi m’mbuyo mukanena zinthu, anthu angasiye kukudalirani. Ntchini: Munthu woliza mkonono. Chitsanzo: (1) Akagona amangokhala ngati ntchini. (2) An- thu a kwawo onse ndi mitchini. Ntchintchi: Mawu okuluwika kapena ophiphiritsa. Chitsanzo: Titakumana naye, anayamba kuimba nyimbo ya ntchitchi ndipo ife tinadziwiratu kuti pakati pathu pali kanthu. Ntchirichiri: Chidikhodikho. Chitsanzo: Mumwetseni madzi mwanayo, akupanga ntchirichiri. Ntchito yabule: Ntchito yopanda malipiro. Chitsanzo: Angondigwiritsa ntchito yabule. Ntchito yakalavulagaga: Ntchito yovuta kwambiri, yole- metsa, ntchito yopweteka kwambiri. Chitsanzo: (1) Ukaphunzira kwambiri, sugwira ntchito ya- kalavulagaga. (2) Anamugamula kuti akapite kundende komanso akagwire ntchito yakalavulagaga. Ntchito yapwitika: Ntchito yopanda malipiro. Chitsanzo: Anthu amenewa amangondigwiritsa ntchito yapwitika. Ntchito yokhetsa thukuta: Ntchito yowawa, yofuna mphamvu. Chitsanzo: Tsiku lililonse ndimakhalira kugwira ntchito yokhetsa thukuta. Ntchito yolemetsa: Ntchito yowawa, ntchito yotopetsa. Chitsanzo: Kukumba chimbudzi ndi ntchito yolemetsa. Ntchito yolimba: Ntchito yovuta, ntchito yopweteka. Chitsanzo: (1) N’chifukwa chiyani mwandipatsa ntchito 301