Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 301
Paphata pa Chichewa
Nsima yolumpha moto: yosapsa.
Chitsanzo: Mwaphika nsima yolumpha moto.
Nsima yosipa: Nsima yopanda ndiwo.
Chitsanzo: Ndinamupeza akudya nsima yosipa.
Nsima yoti kugendera galu kulira: Nsima yolimba
kwambiri.
Chitsanzo: Tinaphika nsima yoti kugendera galu kulira.
Nsompho: Kankhwanga kosemera komwe amakapanga
ngati kakhasu.
Chitsanzo: Ndani waba nsompho wanga?
Nsonga:
(a) Kunsinde, kumapeto kwa chomera.
Chitsanzo: Akudya nsonga za mzimbe.
(a) Ndemanga yakumapeto.
Chitsanzo: Mukufuna kupereka nsonga?
Nsonga: Ndemanga. Tanthauzo lake lenileni ndi kumapeto
kwa chinthu monga nzimbe, mtengo, bere ndi zina.
Chitsanzo: Ndifuna nditsirirepo kansonga.
Nsoti: Mkazi, mtsikana.
Chitsanzo: Mukafunsa nsoti, mupita kubanja ilo.
Nsunamo: Nkwiyo.
Chitsanzo: Ndinawapeza atachita nsunamo.
Nsungwi yamtuwa: Mlongo wako.
Chitsanzo: Mlamu amakwiya kukabwera nsungwi yamtu-
wa.
Nsungwi: Wamtali kwambiri.
Chitsanzo: Taonani pamene walekezopo, kodi ukulowera
kuti mwambamo? Ndiwetu nsungwi bwanawe.
Ntchembere: Mayi yemwe anaberekapo mwana.
Chitsanzo: Ntchembere za pamudzi pano ndi zamabodza.
Ntchembere: Mzimayi makamaka amene anaberekapo.
Chitsanzo: Ntchembere ndi zimene zimakhala ndi
300