Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 30

Paphata pa Chichewa Chibwenzi chanseri: Chibwenzi chobisa. Nthawi zambiri munthu amakhala ndi chibwenzi chimenechi ali ndi mkazi kale. Chitsanzo: Bambowa ali ndi chibwenzi chanseri. Chibwenzi: Mwamuna ndi mkazi omwe amakondana, omwe akufuna kuti adzakwatirane. Chitsanzo: Anthuwa ali pachibwenzi. Chibwibwi: Kudodoma, kulephera kuyankhula bwinobwino chifukwa cha matenda, chibadwa, kapena kusokonezeka ndi zinazake. Chitsanzo: Amachita chibwibwi. Chichewa chagwadagwa: Chozama. Chitsanzo: Akuyankhula Chichewa chagwadagwa. Chichewa chitalichitali: Mawu ozama. Chitsanzo: Atakwiya anayamba kuyankhula chichewa chitalichitali cholukana ndi mwano. Chichewa: Amatanthauza zoyankhula, zonena kapena mawu. Chitsanzo: (1) Ndikusowa chichewa choti ndingawauze. (2) Anthu aja anasemphana chichewa. Chichiri: Chipilala. Chitsanzo: Akufuna kumanga chichiri pokumbukira anthu omwe anamenyera ufulu wa dziko lino. Chidakwa: Woledzera. Chitsanzo: Mtsikana wabwinobwino uja anakwatiwa ndi chidakwa. Chidamuyabwa chitedze: Adatenga matenda. Chitsanzo: Alamwanu ajatu chidawayabwa chitedze. 29