Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 3

Paphata pa Chichewa Abathwa: Mawuwa amanenedwa monyoza anthu omwe ndi aafupi. Dzinali lanayamba chifukwa cha mtundu wina wa anthu akale omwe ankakhala afupiafupi. Anthuwo ankatchedwa abathwa. Chitsanzo: Sindimafuna kuti ana anga adzakwatiwe ndi abathwa. Achabechabe: Opanda ntchito. Chitsanzo: Anthu amene aja ndi achabechabe. Achinansi: Anthu owadziwa, achibale. Chitsanzo: Uziyankhula bwino ndi alendo ungadzanyoze achinansi. Achitaiko (otaika): Anthu osokonekera. Chitsanzo: Muzilalikira anthu achitaiko. Adaminirako: Adaipitsako, anachita zoipa n’kuthawa. Chitsanzo: Amakana kupita kumudzi chifukwa adaminirako. Adamulenga: Adasiya kuyenda naye. Chitsanzo: Anthu amenewa ankagwirizana poyamba, koma pano adalengana. Adanka: Adapita. Chitsanzo: Akuluakulu andanka kumanda ndi nzeru zawo zomwe. Adapinama: Adasintha khalidwe. Chitsanzo: Poyamba mwamunayo ankakalipira mkazi wakeyo, koma pano adapinama moti nayenso amabweza zibakera. 2