Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 299
Paphata pa Chichewa
Nsalu ya lekaleka: Mwana wakhanda. Mawuwa amagwir-
itsidwa ntchito chifukwa makolo ambiri salola kuti mwana
wakhanda anyamulidwe ndi aliyense kuopera ku-
mupweteka. Akaona wina akufuna kumunyamula ama-
muuza kuti leka, usamugwire.
Chitsanzo: (1) Banja la Achisale lagula nsalu ya lekaleka.
(2) Mwamunayo wakwatiranso chifukwa akufuna nsalu ya
lekaleka.
Nsalu yasilika: Nsalu yotelera.
Chitsanzo: Ndani wagula nsalu yasilikayi.
Nsambi:
(a) Kudziwa kusambira.
Chitsanzo: Mwanayu amadziwa nsambi.
(b) Mawuwa amanenedwa wina akakhala kuti walakwa.
Chitsanzo: Nsambi, mungamutsine mwana choncho!
Nsanamila:
(a) Mtengo womwe amaimikira denga kuti lisagwe.
Chitsanzo: Muzike nsanamila.
(b) Munthu wodalilika.
Chitsanzo: Bambowa ndi nsanamila ya pamudzi pano.
Nsanamila: Munthu wodalilika.
Chitsanzo: Bamboyu ndi nsanalila ya mpingowu.
Nsanamirakande: Nkhumba.
Chitsanzo: Bizinezi ya nsanamirakande ndi yotentha
masiku ano.
Nsangala: Waubwenzi.
Chitsanzo: Alendo amafunika kuwalandira mwansangala.
Nsangalatsi: Munthu amene amasangalatsa anthu monga
wazisudzo kapena woimba.
Chitsanzo: Anthu anabwera mwaunjinji kudzatsanzikana
ndi nsangalatsi wawo.
Nsangamutu: Mpango womwe anthu amamanga kumutu
pamaliro kapena akamadwala.
298