Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 298

Paphata pa Chichewa Nkuna: Nsapato. Chitsanzo: Wavala kankuna kakuda. Nkunkhuniza: Bodza lalikulu, kukokomeza. Chitsanzo: Akunenalo ndi bodza la nkunkhuniza. Nkwiyo wosaneneka: Kukwiya kwambiri. Chitsanzo: Ndili ndi nkwiyo wosaneneka. Nong’ona: Yankhula mwapansipansi. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani ukunong’ona? Nong’oneza bondo: Kudandaula utapeza mavuto chifu- kwa chosamva. Chitsanzo: (1) Anyamata amene anasiya sukulu lero akunong’oneza bondo. (2) Zimene mukuchitazi mudzanong’oneza nazo bondo. Nong’oneza nkhani: Mwina chifukwa cha mantha, anthu ena anawuzana nkhani mwachinsinsi n’cholinga choch- enjezana. Chitsanzo: Tabwerani ndikunong’onezeni pang’ono. Noninoni: Zokwanira bwino mafuta. Chitsanzo: (1) Pamene amabwera kuphwandoko pakamwa pake panali noninoni. (2) Ndiwo zake ndi zanoninoni. Nsakanizo wakupha: Zinthu zoti sizingayendere limodzi. Ngati zitayendera limodzi pakhoza kukhala mavuto aaku- lu. Chitsanzo: (1) Umene mukupanga apawu ndi nsakanizo wakupha, zikhoza kukutsegulani m’mimba zimenezo. (2) Umbuli ndi khama ndi nsakanizo wakupha. Nsakanizo woopsa: Zinthu zoti sizingayendere limodzi. Ngati zitayendera limodzi pakhoza kukhala mavuto aaku- lu. Chitsanzo: (1) Umene mukupanga apawu ndi nsakanizo woospa, zikhoza kukutsegulani m’mimba zimenezo. (2) Umbuli ndi khama ndi nsakanizo woopsa. 297