Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 297

Paphata pa Chichewa (b) Chifunga, chizirezire. Chitanzo: Kunjaku kwachita nkhungu. Nkhunguni: Womana. Chitsanzo: Abambo amenewa ndi nkhunguni, amachoka pakhomo ngati alibe kalikonse, n’kupita kukamtini kukagula tiyi ndi chikonda moyo chake. Nkhuntha: Kupusa. Chitsanzo: Nkhuntha imeneyi adzaichenjeretsa anzake. Nkhutukumve: Munthu wosamva, wongotsata zake zo- kha. Chitsanzo: (1) Pasukulu pano sitifuna nkhutukumve. An- thu okhawo amene abwerera sukulu ndi amene angakhale pano! (2) Mwana uyu ndi nkhutukumve. Nkhwangwa pamwala ga: Kukanitsitsa. Chitsanzo: Atamupempha kuti apite anangoti nkhwangwa pamwala ga! Nkhwangwa yatema bondo: Zachitika pabanja pomwepo. Chitsanzo: Mlandu wake ukhala wovuta kuweruza chifukwa nkhwangwa yatema bondo. Nkhwesa: Kusafuna kumva za anzawo kapena liuma. Chitsanzo: Amuna awo anyanya nkhwesa. Nkhwidzi: Mtima woipa, mtima womangofuna zonse zikhale zako. Chitsanzo: Akazi anu ndi ankhwidzi. Nkhwirikwinya: Mbaala zomwe zimabwera chifukwa chowotha moto. Chitsanzo: Mkazi woyera safunika kumaotha moto poopa nkhwirikwinya. Nkhwiru: Wokonda kudya nyama, wosakonda masamba. Chitsanzo: Mwanayu ndi wankhwiru. Nkulukulu: Munthu wamkulu. Chitsanzo: Zoona munthu nkulukulu angamayende osavala mwado! 296