Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 296
Paphata pa Chichewa
Nkhuku ya pamazira: Kupupuluma kapena kuvuta.
Nkhuku ya pamazira imakhala yovuta kwambiri chifukwa
imaona ngati munthu akufuna kutenga mazira ake.
Chitsanzo: Saugwira mtima, amangokhala ngati nkhuku
ya pamazira.
Nkhuku yachikuda: Nkhuku yalokolo.
Chitsanzo: Atiphikira nkhuku yachikuda.
Nkhuku yachizungu: Nkhuku yahaibulidi.
Chitsanzo: Sindidya nkhuku zachizungu.
Nkhuku yoweta sagula pamsika: Mkazi sapeza moyenda.
Mawuwa anabwera chifukwa nthawi zambiri nkhuku
zimene amagulitsa pamsika zimakhala ndi vuto, zina
zimakhala kuti zikudwala kapena zameza singano.
Chitsanzo: Ndinawauza achimwene kuti nkhuku yoweta
sagula pamsika.
Nkhulang’ona: Munthu wolimba mtima.
Chitsanzo: Kugwira ntchito ngati zimenezi kumafuna
nkhulang’ona.
Nkhuli (nkhwiru): Kususukira nyama, kukonda nyama
osati masamba.
Chitsanzo: Anawa ndi a nkhuli.
Nkhumano: Kukumana, malo amene pakumana misewu,
malo omwe anthu amakumana.
Chitsanzo: (1) Lero kuli nkhumano. (2) Tikakumane pa
nkhumano.
Nkhumbzi: Munthu wakuba.
Chitsanzo: (1) Chenjerani naye ameneyu akuyeretsani
m’maso. Ndi nkhumbzi. (2) Mukusungira nkhumbzi pakho-
mo panu pano.
Nkhungu:
(a) Munthu wopusa kapena kuti wopepera.
Chitsanzo: Nthawi zambiri munthu amene amaseka
choncho amakhala nkhungu.
295