Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 295

Paphata pa Chichewa Nkhomaliro: Chakudya chamasana. Chitsanzo: Tiyeni tikachite nkhomaliro. Nkhondo ndi anansi: Mawuwa amatanthauza kuti anza- ko ndi amene amakuchitira chipongwe nthawi zina. Chitsanzo: Andiukira ndithu ngati sakundidziwa, nkhondo ndi anansi ndithu. Nkhongo gwa! Mawu achipongwe onena za munthu wopanda mnzeru kapena wosamva. Chitsanzo: Tachioneni, chili nkhongo gwa, chikupitabe komweko ngakhale kuti dzulo anachiphovomora. Nkhono: Mawuwa amanena za munthu amene amachita zinthu mochedwa kwambiri ngati mmene imachitira nkhono. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani mwatuma nkhono ija. Nkhonya (nkhonyo): (a) Kumenya munthu ndi kuseri kwa chibakera chokunga, kapena zala zopinda. Chitsanzo: Anamukhoma nkhonya n’kumufunsa kuti, “Lota, wakumenya ndani?” (b) Masewera omenyana ndi zibakera. Chitsanzo: Katswiri wina wochita masewera a nkhonya anauza mnzake kuti akamabwera kudzamenyana naye atengeretu bokosi lake. Nkhonya yobwezera kuwawa: Mnzako akamakubwezera zimene unamuchitira umamva kupweteka kwambiri. Chitsanzo: Unandichitansotu zomwezi, kungoti khonya yobwezera imawawa! Nkhope itatembenuka: Nkhope itasintha. Chitsanzo: Ndinawapeza nkhope itatembenuka. Nkhope yachikoka: Nkhope yokongola. Chitsanzo: Mwanayu ali ndi nkhope yachikoka. 294