Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 294

Paphata pa Chichewa Nkhalwe: Nkhanza. Chitsanzo: Bambowa ndi ankhalwe, amamenya akazi awo. Nkhandwe: Munthu wachinyengo, wokonda kuchen- jeretsa anzake. Chitsanzo: Sindimadziwa kuti mwamuna wake uja ndi nkhandwe. Nkhani ndi kamnyamata: Nkhani sichepa. Chitsanzo: Mukuti chiyani? Pajatu nkhani ndi kamnyama- ta! Nkhani yagona pati: Kodi vuto lili pati? Chitsanzo: Mpofunika tidziwe kuti kodi nkhani yagona pati. Nkhani yochititsa nyansi: Nkhani yosakondweretsa, yonyansa. Chitsanzo: Ndangomva nkhani yochititsa nyansi. Nkhani yodetsa kukhosi: Nkhani yosakondweretsa, yo- detsa nkhawa. Chitsanzo: Ndangomva nkhani yodetsa kukhosi. Nkhata: (a) Maluwa omwe anthu amaika pamanda. Chitsanzo: Amagulitsa nkhata za maliro. (b) Chinthu chimene munthu amaika pamutu kuti chimene wasenza chisamamugogode. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani wasenza popanda nkhata? Nkhatayagwa: Munthu wosakonda ntchito. Chitsanzo: Mtsikana ameneyu ndi nkhatayagwa. Safuna kugwira ntchito koma kudya basi. Nkhatheya: Munthu waluso pa ntchito yake, munthu wolemekezeka. Chitsanzo: Kwabwera mikhatheya ya zomangamanga. Nkholokolo: Munthu woyambanitsa anthu. Chitsanzo: Anthu sati ayambana liti pamudzi pamene paja. Ndikuganiza kuti pali nkholokolo. 293