Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 293

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Sindimadziwa kuti ndikuthawa njokaluzi. (2) Sangakumenyeni, iwowaja ndi njokaluzi. Njole: Mkazi wokongola Chitsanzo: Nawenso upeze kanjole kako. Njombwa: Ndalama. Chitsanzo: Mwanayu wangochepa, koma amapeza njomb- wa. Njonda: Bambo. Chitsanzo: Njonda inayake imafuna kumugwiririra. Njovu: Munthu wonenepa kwambiri. Chitsanzo: Mayi awo ndi njovu. Nkadza apo ndaima: Mawu amene anthu amakonda kunena akakhala kuti akumaliza kuyankhula makamaka pamlandu. Chitsanzo: Basitu, tsiku lina ndinangoona abweranso, ndiye ine ndikanatani? Basi ndinangowalandira. Nkadza apo ndaima! Nkhakamila: Munthu wokakamira. Chitsanzo: Mwana ameneyu ndi nkhakamira. Nkhalamba yogwa n’kumina: Nkhalamba yotheratu, munthu wokalamba kwambiri. Chitsanzo: Pamudzi apa pali nkhalamba zogwa n’kumina. Nkhalamo: Wankhanza. Chitsanzo: Mayi amenewa ndi nkhalamo, amazunza ana a anzawo. Nkhali yadooka (nkhali yabooka): Mkazi wam’fera, akazi awo amwalira. Chitsanzo: Bambo amenewa nkhali yawo inadooka. Nkhali: Mkazi. Chitsanzo: Ndikufuna udzakhale nkhali yanga! 292