Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 292
Paphata pa Chichewa
Nje: Kulibe, sizitheka.
Chitsanzo: “Kodi munthu uja wabwera?” “Nje!”
Njenjenje (kunjenjemera): Kugwedezeka chifukwa cha
mantha kapena matenda.
Chitsanzo: Ndinawapeza ali njenjenje.
Njenjete: Munthu wadyera. Mawuwa anachokera ku ka-
chilombo komwe kamadya zovala.
Chitsanzo: (1) Njenjete zamudyera zovala. (2) Mwanayu
ndi njenjete.
Njerengo: Nkhani zongopeka.
Chitsanzo: Amakonda kukamba njerengo.
Njirayachepa: Wamatekenya, wopotoka mapazi.
Chitsanzo: (1) Kukubwera njirayachepa. (2) Njirayachepa
uja ali kuti?
Njodo: Mimba yaikulu, yangati kamtsuko.
Chitsanzo: Ambiri omwe amamwa wamasese amakhala
ndi njodo.
Njoka muudzu: Mawuwa amanena za munthu wachiny-
engo komanso woipa amene amakonzera anzake chiwem-
bu.
Chitsanzo: Ali ngati njoka muudzu, podutsana amandim-
wetulira koma mumtima muli tho dzimilandu.
Njoka:
(a) Munthu woipa.
Chitsanzo: Pamene miyezi iwiri inkatha, mpamene ndina-
zindikira kuti mkazi uja ndi njoka.
(b) Munthu wosakonda kumwa madzi.
Chitsanzo: Mwana ameneyu ndi njoka.
Njokaluzi: Munthu wopanda mphamvu. Njokaluzi ndi
chikopa chimene chimatsala, njoka ikufundula. Nthawi zi-
na anthu amatha kuthawa chinthu chimenecho poganiza
kuti ndi njoka yeniyeni.
291