Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 291
Paphata pa Chichewa
Ngolowera: Kuwirira chifukwa cha udzu kapena
chimanga.
Chitsanzo: Musiye kudutsa njira zachidule, kunjaku
kwachita ngolowera.
Ngongole: Kubwereka ndalama kapena zinthu zamwini.
Chitsanzo: Ngongole imakoma potenga koma pobweza
imawawa.
Ngozi: Maliro.
Chitsanzo: Tathokoza kwambiri chifukwa choti
mwatilondola mutamva za ngozi yatigwerayi.
Nguli: Ndi kamtengo komwe kamakhala kosongoka mbali
imodzi. Kamtengoka amakagwiritsa ntchito pochita
masewera. Amakakwapula ndi lamba ndipo kamazunguli-
ra.
Chitsanzo: Akungozungulira ngati nguli.
Nguwi (nkhufi): Chakudya chikakhalitsa chimamera
nguwi, nthawi zinanso zovala zomwe zili pachinyezi
zimamera nguwi.
Chitsanzo: Nsima ya dzana ija yapanga nguwi.
Ngwazi: Munthu wamphamvu, wotchuka, katswiri.
Chitsanzo: Mwamuna ameneyi ndi ngwazi pankhondo.
Nimurode: Munthu woipa kwambiri. Baibulo limatchula
za munthu ameneyu kuti ndi amene anali woyambirira
kukhala ndi mphamvu zambiri padzikoli komanso anali
wankhanza kwambiri.
Chitsanzo: Wapita kuti Nimurodi uja?
Ninkha nyenwa: Kulonjeza chifukwa chofuna kutsan-
galatsa ena.
Chitsanzo: Andale a masiku ano akumangotininkha nyen-
wa.
Njala inatipha: Njala inatipweteka kwambiri.
Chitsanzo: Tinakhala tsiku lonse osadya moti njala
inatipha!
290