Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 290
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: (1) Zoonadi, ng’oma yolira kwambiri sichedya
kusweka. Taonani wasiya ana amayereyere. (2) Mnyamata
amene uja ndi ng’oma pankhani ya zisudzo.
Ng’oo! Mawu omwe amanenedwa munthu wina akamauza
mnzake kuti walephera, wauponda.
Chitsanzo: Ngati umaganiza kuti uipeza itapsa, ng’oo!
Ng’ung’udza: Yankhula mwapansipansi, kuchita mwano.
Chitsanzo: (1) Ndani akung’ungudza kuseriko? (2) Mwana
uyu amang’ung’udza ukamamutuma.
Ngala: Maso a tirigu.
Chitsanzo: Osamapulula ngala za tiligu zisanakhwime.
Ngamila: Munthu wosakonda kumwa madzi, koma akati
amwe amawamwa kwambiri.
Chitsanzo: Bambo anu ndi ngamila.
Nganga:
(a) Munthu wokalamba, nkhalakale.
Chitsanzo: (1) Kodi anganga aja apita kuti? (2) Nganga
zonse zinatha kumwalira.
(b) Chidale, chifuwa.
Chitsanzo: Mpirawo anauika panganga.
Nganganga: Osafuna kusiya kapena kusintha.
Chitsanzo: Nthawi zonse amangoti nganganga pa zimene
akudziwa, safuna kusintha maganizo.
Ngaphwete: Makonda kuseka.
Chitsanzo: Anawa ngaphwete.
Ngenge (dzuwa zii): Mtsikana wokongola kwambiri.
Chitsanzo: (1) Ndagwira kangenge kenakake. (2) Ku-
kubwera dzuwa zii.
Ngodya: Pakona.
Chitsanzo: Mwala umene amisiri anaukana unasanduka
wapangodya.
289