Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Seite 29

Paphata pa Chichewa Chibaluwa: Kalata. Chitsanzo: Ndikuganiza zowalembera chibaluwa. Chibenga: Chitsiru. Mawu amenewa amagwira ntchito tikamanena za munthu yemwe ndi wopanda nzeru mpang’ono pomwe. Chitsanzo: Achimwene anu aja ndi chibenga. Chibengere: Chitsiru Chitsanzo: Kumalemekeza zibengere kuti upewe phokoso. Chiboli: Chilombo chomwe chimaoneka mowala chifukwa chilibe ubweya. Anthu amanena mawuwa ponena za munthu amene wametetsa mpala. Chitsanzo: Kodi ziboli zija zadutsa apa? Chiboliboli: Munthu wopanda nzeru yemwe akakhala pagulu amangokhala duu. Tanthauzo lake lenileni ndi chinthu chosema pofanizira chinachake. Chitsanzo: Chapita kuti chiboliboli chija? Chibufumpweya: Chinthu chopanda kanthu, chiphwafu. Chitsanzo: Banzi limene anandipatsa linali chibufumpweya. Chibwana cha nchombo lendee: Chibwana chachikulu. Chitsanzo: Chimene akuchitachi ndi chibwana cha nchombo lendee! Chibwana chimatuma: Mawuwa amanenedwa ngati munthu wachita zinthu chifukwa chosaganiza bwino kenako n’kumadandaula. Chitsanzo: Sindinakuuzeni kuti chibwana chimatuma? 28