Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 289

Paphata pa Chichewa (b) Kupusa. Chitsanzo: Munthu wake amangoti ndungundu. Nduu: Mulu, kuunjikana. Chitsanzo: Ndinapeza zovala zakuda zili nduu! Ndwii: Mmene munthu amaonekera akakhumudwa kapena akamasowa chochita. Chitsanzo: Ndinawapeza ali ndwii pakhonde. Neng’a: Kukhala pampando kapena pabedi kwinaku ukumva bwino. Chitsanzo: Ndinamupeza ali neng’a, pampando. Ng’amba chipika: Waza nkhuni. Chitsanzo: Anyamata amphamvu apite kuseriku kuti akang’ambe zipika. Ng’amba khofi: Kupatsa munthu wina khofi mwamphamvu. Chitsanzo: Mayiwa awang’amba khofi amuna awo. Ng’amba kukamwa: Kuyankhula kwambiri, kuyankhula kapena kulira mokweza kwambiri. Chitsanzo: (1) Ukufuna ndichite kung’amba kukamwa kuti umve! (2) Kodi ndi ndani akung’amba kukamwayo? Ng’amba: (a) Chilala Chitsanzo: Amene atapulumuke ng’amba imeneyi ndi mwamuna. (b) Kuona zoopsa. Chitsanzo: Amachita masewera ndi njuchi, ndiye zamuonetsa ng’amba. Ng’anjo: Moto waukulu. Chitsanzo: Sitimakazinga chimanga ndi ng’anjo, chimatha ndi kupserera. Ng’oma: Munthu wotchuka kapena wodziwika kwambiri. Mawuwa anayamba chifukwa ng’omba imamveka patali. 288