Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 288

Paphata pa Chichewa Ndondocha: Munthu wamimba youma ngati mpira, mun- thu wodya kwambiri. Mawuwa anayamba kuchokera ku zikhulupiriro zoti afiti amatha kusunga tianthu ta mimba zikuluzikulu kuti aziwagwirira ntchito kapena kuwalimira m’munda. Chitsanzo: (1) Mwana wanuyu amadya ngati ndondocha. (2) Ana awo onse ndi ndondocha. Ndondola: Yenda mofulumira ngati mbalame. Chitsanzo: Akundondola kulowera uku. Ndondoli: Malovu omwe akuyoyoka kapena kuchucha kuchokera pakamwa. Chitsanzo: Ngakhale utakhala kuti umagwetsa ndondoli sindingakusiye. Ndondomeko: Dongosolo lake, mwatsatanetsatane. Chitsanzo: Ukamachita zimenezi umafunika kutsatira ndondomeko yake. Nduke: Akazi okongola. Chitsanzo: Mtauni mumakhala nduke zosalitsa tulo. Ndulu: Chinthu chowawa chimene chimapezeka mkati mwa nkhuku komanso zinthu zina. Anganenedwe ponena kuti chinachake ndi chowawa kwambiri. Chitsanzo: Mankhwalawa ndi ndulu. Ndundu: Anthu ovuta. Chitsanzo: Ndundu zachoka, tsopano timasuke. Ndundundu (ndu): Kudzadziratu, zambiri. Chitsanzo: Mchenga wangoti ndundundu pakhonde. Ndundundu: Zambirimbiri. Chitsanzo: Tinapeza chimanga chili ndundundu m’nyum- bamo. Ndungundu: (a) Kungokhala ndwii, kukwiya. Chitsanzo: Kumasekako, osamangokhala ndungundu! 287