Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 287
Paphata pa Chichewa
pakhomo pano!
Ndikupanga masamu: Ndikuganiza zochita.
Chitsanzo: Ndikupanga masamu a mmene ndingapezere
ndalama zogulira foni imeneyi.
Ndilekere? Chondiletsa n’chiyani?
Chitsanzo: “Upita kudansi?” “Ndirekere?”
Ndilibe nawo mawu: Amandisowetsa chonena.
Chitsanzo: Ana anuwa ndilibe nawo mawu.
Ndilije: Mawu okokomeza ponena kuti ulibe.
Chitsanzo: Ine vuto ndilije, ali nalo ndi amene aku-
werewetawo.
Ndimangokuyang’anani: Ndimangokusiyani, ndimadziwa
kuti mukumana nazo.
Chitsanzo: Inetu ndimangokuyang’anani, ndimadziwa kuti
zikavuta mubwera.
Ndimbwandimbwa: Kamvekedwe ka kufewa kwa chinthu.
Chitsanzo: Matilesiwo amangoti ndimbwandimbwa.
Ndimuthira dothi m’khutu: Ndikupha.
Chitsanzo: Akachita masewera ndimuthira dothi m’khutu.
Ndindindi: Anthu ambiri, kuwirira.
Chitsanzo: (1) Pakhomo pawo mitengo inangoti ndindindi.
(2) Ndinapeza anthu ali ndindindi pakhomopo.
Ndipsi: Munthu wochita zoipa zosadziwika kwa anthu.
Chitsanzo: Musawaone kutchena kuja, iwowajatu ndi
ndipsi.
Ndithane nazo: Kungochita kuti umalize basi.
Chitsanzo: Ndimangochita kuti ndithane nazo.
Ndiweyani: Waukulu.
Chitsanzo: Kunjaku kuli mdima wa ndiweyani.
Ndodomtolo: Osadziwa chochita kapena chonena.
Chitsanzo: Nditamva zimene amanena, ndinangoti
ndodomtolo.
286