Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 286
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: (1) Madzi a mutsukowo amangoti
ndengundengu. (2) Ndimachita mantha bwato likayamba
kuchita ndengundengu.
Ndevu za ponya mtedza upaone: Ndevu zochuluka zedi
zodzadza pachibwano komanso m’masaya.
Chitsanzo: Bambo ake ali ndi ndevu za ponya mtedza
upaone.
Ndevu zampanda: Ndevu zochuluka zedi zodzadza pa-
chibwano komanso m’masaya.
Chitsanzo: Bambo ake ali ndi ndevu zampanda.
Ndewu ya phwee: Ndewu yoopsa.
Chitsanzo: Mtchalitchi mukumachitikanso ndewu ya
phwee!
Ndewu yafumbi: ndewu yoopsa.
Chitsanzo: Kumsikaku kunali ndewu yafumbi.
Ndewu yamtima bii: Ndewu yoopsa.
Chitsanzo: Kutchalitchiku kunali chindewu chamtima bii.
Ndi mwalamwala: Ndi wolimba, wodalilika, wamphamvu.
Chitsanzo: (1) Mwana ameneyu ndi mwalamwala,
sangaledzere ndi kapu imodzi. (2) Agogowa ndi
mwalamwala, amalima ngati adakali mnyamata.
Ndi patali: Waluso kwambiri.
Chitsanzo: Amene uja ndi patali, sungamupose kutha-
manga.
Ndi ulendo: Mawuwa amanenedwa potamanda munthu
yemwe amachita zinazake mwaluso. Kunena kwina timati
“si masewera.”
Chitsanzo: Mwana uyuyu ndi ulendo!
Ndi wautali: Kuyenda ulendo wautali.
Chitsanzo: Ndikangomaliza kugwira ntchito, ndi waulali.
Ndigwira mtengo wanji: Nditani ine?
Chitsanzo: Ndigwira mtengo wanji mukandithamangitsa
285