Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 285

Paphata pa Chichewa Ndanenandanena: Wosamva za ena. Chitsanzo: Bwana amene aja ndi ndanenandanena. Ndangodutsamo sindinatchole nkhwani: Ndangonena, sindinapalamule mlandu. Chitsanzo: Kodi mukuwanena achimwene anu eti? Ayi, inetu ndangodutsamo sindinatchole nkhwani. Ndapota nanu: Pepani, ndikukupemphani. Chitsanzo: Ndapota nanu, ndikhululukireni. Ndapotananu: Kuchonderera. Chitsanzo: Ndapotananu, ndikhululukireni. Ndauyambatu: Mawuwa amanenedwa munthu akaman- yamuka pamalo. Chitsanzo: Ndauyambatu, mundipeza! Ndawachita zinthu: Ndawalanga. Chitanzo: Ana amwano aja ndawachita zinthu. Ndazitayira kudzala: Ndakhululuka. Chitsanzo: Zonse zomwe anandichitira ndazitayira kud- zala. Ndaziyesa dzala: Ndakhululuka. Chitsanzo: Zonse zomwe anandichitira ndaziyesa dzala. Ndege: Botolo lothandiza anthu kudziwa kuti mowa wapsa (makamaka kachaso). Chitsanzo: Wapsa kumtundaku. Ndaonera ndege pansewupo. Ndekesha: Chikabudula chachikulu, chithewera. Chitsanzo: Akamalima amavala ndekesha. Ndendende: Kuchitika momwemo, osatsala chilichonse. Chitsanzo: Ulosiwo unakwaniritsidwa ndendende. Ndengundengu: Kugwedezeka kwa madzi kapena zinthu zamadzimadzi, kugwedezeka kwa chinthu chomwe chili pamadzi. 284