Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 284

Paphata pa Chichewa Ndadya njinga: Mawuwa amanenedwa zikakhala kuti munthu akunenetsa kuti sangachite zimenezo. M’mawu ena angatanthauze kuti n’zosatheka. Chitsanzo: Sindigayerekeze kugulitsa nyumba yanga pokhapokha nditadya njinga. Ndaimika manja: Ndalephera, kugonja. Chitsanzo: Mwamuna ameneyu ayi, ndaimika manja. Ndakhutakale: Munthu wachimimba chachikulu. Chitsanzo: Amageya anyezi ambiri amakhala a ndakhutakale. Ndakhutandalema: Mpando wopangidwa moti munthu amakhala ngati wagona. Nthawi zambiri umapangidwa ndi matabwa ndipo pokhalira amaikapo chisaka kapena nsalu. Chitsanzo: Agogo akhala pampando wa ndakhutandalema. Ndakoka: Ovololo. Chitsanzo: Upemphe abwana ako akugulire ndakoka. Ndakoka: Ovololo. Chitsanzo: Wavala ndakoka. Ndakupukwani: Ndakusowani. Chitsanzo: Ndakupukwani amama. Ndale: (a) Kukola munthu wina kuti agwe. Chitsanzo: Amakonda kutcherana ndale. (b) Zimene anthu amachita poyendetsa dziko. Chitsanzo: Ambiri amayamba ndale chifukwa cha dyera. Ndamuopera: Wandichititsa mantha. Chitsanzo: Ndamuopera, ndi munthu woipa kwambiri. Ndandanda: Zinthu zolembedwa mwadongosolo. Chitsanzo: Talembani ndandanda ya zinthu zimene mukufuna. 283