Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 283

Paphata pa Chichewa ataspa, m’modzi anadya pomwe wina sanadye. Winayo anapusitsa mnzakeyo ngati nayenso adya nawo. Chitsanzo: Ndinadziwa ine kuti akunamizana kudya galu. Namondwe: Mphepo yaikulu ya panyanja. Mawuwa angatanthauzenso mavuto. Chitsanzo: Chaka chatha tinakumana ndi namondwe. Namwali: (a) Mkazi yemwe sanakwatiwe, mtsikana. Chitsanzo: Kunyumba kwa Abengo kuli kanamwali. (b) Munthu amene akuvinidwa, kulowa chinamwali. Chitsanzo: Pakhomo pawo pachoka anamwali atatu. Namwalikande: Nkhumba. Chitsanzo: Atazindikira kuti timadya namwalikande, anasiya kubwera kudzabwereka mapoto. Namwino: Nesi. Chitsanzo: Anamwino akuthawa m’dziko muno chifukwa cha kuchepa kwa malipiro. Namwino: Nesi. Chitsanzo: Boma lalemba anamwino ambiri. Nankungwi: Wolangiza mwana kuti akule bwino. Nthawi zambiri amalangiza mwanayo pachinamwali. Chitsanzo: Mayiwa ndi amene akhale nankungwi wa mwa- nayu pachinamwalipa. Napweri: Munthu woyera kwambiri nthawi zina ndi tsitsi lomwe, alubino. Chitsanzo: Aliyense wotchula alubino kuti napweri azimangidwa. Nchochombe: Munthu waluso kwambiri. Chitsanzo: Imeneyi ndi michochombe yamasamu. Ndachimina: Ndalapa, sindidzabwerezanso. Chitsanzo: Ndachimina, sindidzadzeranso njira imeneyi. 282