Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 282

Paphata pa Chichewa N’chake: Adazolowera. Chitsanzo: Mtsikana amene uja m’chake, sadzasiya kuth- amanga. N’dzasamban’kadzafa: Nkhumba. Chitsanzo: Akufuna ndikawakonzere n’dzasam- ban’kadzafa. N’dzayeran’kadzafa: Nkhumba. Chitsanzo: Akufuna ndikawakonzere n’dzayeran’kadzafa. N’zosachita kufunsa: N’zachionekere, n’zachidziwikire. Chitsanzo: N’zosachita kufunsa kuti nafenso itikhudza njalayi. Nakubala: Munthu yemwe anabereka mwana. Chitsanzo: Mpofunika kumalemekeza anakubala. Namageyaanyezi: Munthu wolemera, wachuma. Chitsanzo: Anamageyaanyezi samangira lamba, koma taye. Namageyaanyezi: Munthu wolemera. Chitsanzo: Kukhala namageyaanyezi kulinso ndi kuipa kwake, umasowa tulo. Namandwa: Katswiri. Chitsanzo: (1) Amenewa ndiye anamandwa a pakampani pano. (2) Ameneyu ndi namandwa pankhani yokonza zi- gayo. Namanyonyolo: Katswiri. Chitsanzo: Ameneyu ndi namanyonyolo pankhani zoimba- imbazi. Namfedwa: Munthu amene wachibale wake wamwalira. Chitsanzo: Anamfedwa onse anauzidwa kuti asayambe kulira mpaka amfumu atadziwitsidwa. Namizana kudya galu: Kuikana m’mavuto, kunamizana. Anthu awiri anauzana kuti aphe galu n’kumudya, koma 281