Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 281

Paphata pa Chichewa Mzamba: Munthu wothandiza azimayi pobereka. Chitsanzo: Mā€™dziko muno muli azamba ochepa. Mzime: Munthu womalizira kubadwa. Chitsanzo: Ine ndinadziwa kuti ndi mzime nditaona zimene ankachita. Zikuoneka kuti anamulerera pachilolo. Mzinda: (a) Malo ochitira chinamwali. Chitsanzo: Kumzinda sikuyenera kufika anthu osavinidwa. (b) Tauni. Chitsanzo: Mzinda wa Lilongwe ndi wosalongosoka. Mzozodo: Alibe munthu wopikisana naye. Chitsanzo: Sungakhale mzozodo pa chilichonse. 280